歌词
Tamvani nonse inu ankhawa ndi kuti mawa ndili ku gawa, ndani amene angaime ndi gulu langa.
Choka wachepa kayamwe kwa amako mphwanga.
Funsani timapanga bwanji, pomwa therere lopanda mchere,
Inetu ndimchokela ku malawi, kadziko kakan'gono koma anthu pwechepweche,
Kamuzu anati anatipeza tili maliseche.
Nyanja ya malawi ndi mapili madambo abwino,
Ndiwachonde, wamtendele Malawi,
Is i ndi mphatso zomwe tilinazo mdziko lathu la malawi.
Inu mwina mwamwayi, mupeza nthawi, mupite mukawoneko
Kwa inu amene muli uko kuja, ndipo munachoka kwanu kale, imvani izi.
Musaiwale, kumene munachokela, osasochela, tidzipita uko kumudzi, kuti tikaone makolo,
Ndalama zimakoma kudya ndi abwenzi komanso makolo
Tikapanga makwacha okwana, enawa tiwatumizile, ndicholinga choti, zakudya, zovala atha kugula, sukulu ana kulipila.
Tiyeni tikalandila malipilowo tisamangomwela.